"MAPOINTSI ATATU PA BANGWE NDI OFUNIKIRA" - MTETEMERA
Mphunzitsi watimu ya Creck Sporting Club, Macdonald Mtetemera, wati achita china chilichonse chotheka kuti apeze chipambano pamwamba pa timu ya Bangwe All Stars pomwe akukumana nawo loweruka poti mapointsi atatu akhale ofunikira kwambiri kutimuyi.
Iye amayankhula patsogolo pa masewerowa omwe aseweredwe pa bwalo la Civo ndipo wati timu yake yakonza mavuto ogoletsa omwe anali nawo ndipo ayesetsa kuti achite bwino.
"Awa ndi masewero ena aja anali amu chikho nde amene aja amakhala ovuta kwambiri koma awa ndi ena nde takonzekera bwino ndipo mapointsi atatu awawa ndi ofunikira kwambiri nde tikawamenyera nkhondo kuti tichite bwino." Anatero Mtetemera.
Iye wati tsopano kutimuyi osewera onse omwe anali ovulala achira ndipo tsopano akhale akusankha osewera abwino kuti akawayimilire pa masewerowa.
Timu ya Creck Sporting Club ili pa nambala yachisanu ndi chimodzi (6) pomwe ili ndi mapointsi 16 pa masewero khumi ndi amodzi (11).
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores