"NDI MASEWERO OVUTA KUTENGERA MMENE TILILI MU LIGI" - YASIN
Mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Rodgers Yasin, wati timu yake ikhale ndi masewero ovuta kwambiri pomwe akukumana ndi Creck Sporting Club poti timuyi ikuvutika mu ligi.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi timuyi pa bwalo la Civo loweruka likudzali ndipo wati timu yake iyesera osewera ena omwetsa zigoli poti zikuvuta kuti zigoli zizibwera.
"Ndi masewero ovuta kutengera pomwe Ife tili mu ligi koma tiyesetsa kuti tikapezeko kenakake. Timu isewera bwino konse koma kuvutika kugoletsa nde tiyesera anyamata ena omwe tilinawo kuti mwina vutoli lithepo." Anatero Yasin.
Timu ya Bangwe All Stars ili pa nambala 14 mu ligi ya TNM pomwe ili ndi mapointsi asanu ndi awiri (7) pa masewero 11.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores