"NDI MASEWERO OFUNIKIRA KWA IFE" - KAUNDA
Mphunzitsi watimu ya Karonga United, Oscar Kaunda, wati timu yake yakonzeka bwino kwambiri kuti ikumane ndi timu ya FOMO poti masewerowa ndi ofunikira kwambiri kutimuyi.
Iye amayankhula patsogolo pa masewerowa omwe aliko loweruka pa bwalo la Karonga ndipo wati angakhale kuti FOMO sakuyidziwa, Iwo sakuyidelera timuyi.
"Tikusewera ndi FOMO anyamata akonzekera bwino kwambiri kuti adzachite bwino, tikuchoka kosewera ndi Mzuzu City Hammers koma inali chikho China apa ndi ligi nde tiyesetsa kuti tichite bwino chifukwa ndi masewero ofunika kwambiri." Anatero Kaunda.
Iye watinso osewera omwe anali ovulala sanachire ndipo akungowapempherera kuti akhale bwino koma agwirizana kuti aziyesetsa kupambana masewero awo mmalo mwa iwowo.
Timuyi ili pa nambala 13 mu ligi pomwe ili ndi mapointsi okwana 12 pa masewero 11 omwe iwo asewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores