"MPIRA NDI WANKHANZA KWAMBIRI" - YASIN
Mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Rodgers Yasin, wati mpira ndi wankhanza kwambiri pomwe umalanga timu imene imataya mipata kwambiri ngati zomwe awona Iwo pabwalo la Karonga loweruka masana.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 2-0 ndi timu ya Baka City ndipo wati timu yake inali ndi mwayi onse kuti apambane komabe chitsogolo chikuoneka chowala.
"Mpira ndi wa nkhanza kwambiri, mwaona mmene tasewera chilichonse chabwinobwino koma taphonya mipata yochuluka zomwe anthu angotilanga nde zapweteka kwambiri." Anatero Yasin.
Iye wati timu yake ayesabe kukonza mavuto awo kuti chilichonse chikhale bwino kuti ayambenso kuchita bwino ndi kusuntha kumtunda kwa ligi.
Timuyi ikadali pa nambala yachikhumi ndi chinayi (14) pomwe ili ndi mapointsi asanu ndi awiri (7) pa masewero khumi ndi amodzi (11).
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores