"NDINE WOKONDWA POTI TAPAMBANA" - CHIRWA
Mphunzitsi watimu ya FOMO FC, Gilbert Chirwa, wayamikira osewera ake kamba kolimbikira kuti apeze chipambano poti wati masewero awo ndi Moyale Barracks anali ovuta kwambiri.
Iye amayankhula atatha masewero omwe apambana 2-1 pa bwalo la Mulanje Park ndipo wati kulimbikira kwa osewera ndikomwe kwawapindulira kwambiri.
"Anali masewero ovuta kwambiri poti Moyale ili ndi ukadaulo wochuluka kwambiri koma anyamata analimbikira kwambiri, sanayang'ane pansi nde ndine wosangalala poti masewero ngati awa tapambana ndekuti tsopano tayamba kukhazikika." Anatero Chirwa.
Timu ya FOMO yafika pa nambala yachisanu ndi chinayi (9) pa masewero khumi ndi amodzi (11) omwe yasewera pomwe ili ndi mapointsi okwana 14.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores