"CHITIPA NDI TIMU YABWINO KOMA TIKUFUNA KUWINA" - MTETEMERA
Mphunzitsi watimu ya Creck Sporting Club, Macdonald Mtetemera, wati timu yake yakonzeka bwino kwambiri kuti ikachite bwino ku Karonga pomwe ikungofunako chipambano chokha basi.
Mtetemera amayankhula patsogolo pa masewerowa lamulungu ndipo wati timu yake ikufunitsitsa mapointsi atatu basi ngakhale sakuwatengera masewerowa mophweka poti ali pansi pa ligi.
"Ndi masewero enanso ovuta poti Chitipa United ndi timu ina yabwino komabe Ife tikuyang'ana zonsezo, tikungokonzekera kuti tikwanitse kutenga chipambano basi." Anatero Mtetemera.
Iye anati timu yawo kufanana mphamvu ndi FCB Nyasa Big Bullets kunawasuntha mu ligi koma ndi masewero osiyana ndi Chitipa United koma akayesetsabe kuti sabata ino apeze chipambano.
Timuyi ili pa nambala yachisanu ndi chimodzi (6) pomwe ili ndi mapointsi 15 pa masewero khumi omwe yasewera mu ligi ya TNM.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores