"TIKUWALIMBIKITSA KUTI TIPEZE CHIPAMBANO" - CHIRWA
Mphunzitsi watimu ya FOMO FC, Gilbert Chirwa, wati timu yake yakonzeka bwino kwambiri ndipo walimbikitsa osewera ake kuti adzakwanitse kupeza chipambano loweruka.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi timu ya Moyale Barracks pa bwalo la Mulanje Park ndipo wati akudziwa kuti Moyale ili ndi ukadaulo wa mu ligi koma ayesetsa kuti apambane mmasewerowa.
"Zokonzekera zathu zayenda bwino ndipo anyamata tawalimbikitsa kuti adzachite bwino mmasewerowa. Tikudziwa kutisewera ndi timu yabwino, achiyambakale mu ligiyi komabe anyamata tawauza kufunika kopambana masewerowa nde takonzeka." Anatero Chirwa.
Timu ya FOMO ikupita mmasewerowa ili pa nambala 13 mu ligi ya TNM pomwe ali ndi mapointsi okwana 11 pa masewero 10 omwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores