"MASEWERO AKHALA OVUTA KWAMBIRI" - YASIN
Mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Rodgers Yasin, wati akudziwa kuti masewero awo ndi timu ya Baka City akhala ovuta poti onse akufunitsitsa atachoka pansi pa ligi koma akukhulupilira kuti achita bwino.
Iye amayankhula patsogolo pa masewerowa omwe ali pa bwalo la Karonga ndipo wati ali ndi chikhulupiliro kuti masewerowa achita bwino pomwe akonza vuto lophonya kwambiri.
"Akhala masewero ovuta kwambiri poti tonse tili pansi nde imakhala ngati tikufuna tithaweko koma ifeyo tikudziwa kufunika kopambana masewerowa, masewero apitawo tinavutika nkhani yomwetsa zigoli koma takonzs ndekuti tikayambira pomwe tinalekezekera ndi Hammers." Anatero Yasin.
Iye wati wakonza tsopano mavuto awo osamwetsa zigoli ndipo ali ndi chikhulupiliro chonse kuti mmasewero awo apambana.
Timu ya Bangwe ili pa nambala 14 mu ligi ya TNM pomwe ili ndi mapointsi okwana asanu ndi awiri (7) pa masewero khumi (10) omwe iyo yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores