NKHULAMBE ABWERERA MCHIGAWO CHACHIWIRI CHA LIGI
Katswiri wakale watimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Collen Nkhulambe, wati akuyembekezera kubwereranso mu bwalo la zamasewero mu chigawo chachiwiri cha ligiyi pomwe wati tsopano alibwino.
Iye watsimikiza nkhaniyi kwa Owinna itamufikira za kusaoneka kwake kuyambira mchaka cha 2023 ndipo iye wati anavulala koma tsopano alibwino.
"Mpira sindikuponya kaye chifukwa cha zovuta ndinakumana nazo mu nkhani ya mpira chifukwa ndinakhala chaka ovulala nde pano ndikuzitolera pang'onopang'ono koma pano ndilibwino mutiwonanso posachedwapa." Anatero Nkhulambe.
Ngakhale akuti abwerera posachedwa, iye wati palibe timu yomwe yamufikira kapena kukambirana nayo poti osewera akakhalitsa osasewera matimu ambiri amamukayikira ndipo zonse wasiya mmanja mwa Mulungu.
Katswiriyu yemwe anagoletsa chigoli pa masewero oyamba apabwalo la Bingu watsimikiza kuti mphamvu zake ndi luso ndi lomwe anali nalo mmbuyomu ndipo akadzakhazikika azachitanso bwino ngati kale.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores