"TIKUFUNANSO MAPOINTSI ATATU ENA KU BLANTYRE" - MPONDA
Mphunzitsi watimu ya Silver Strikers, Peter Mponda, wati timu yake ikuonetsa mphamvu zina zoonjezera kutsatira kusasewera kwa masabata atatu ndipo apanga zoti akapambanenso ku Blantyre.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi timu ya Mighty Waka Waka Tigers pa bwalo la Kamuzu lolemba ndipo wati timu yake yakonzeka kwambiri kuti ichite bwino mmasewerowa.
"Akhala masewero abwino kwambiri ndipo anyamata onse alibwino kuonetsa kuti akonzeka kuchita bwino nde tinabwera ku Blantyre tinapambana ndi Bullets apanso tikufunitsitsa kuti tikatengenso mapointsi atatu ena ku Blantyre." Anatero Mponda.
Iye watinso timu yake mwina ikhonza kusokonekera ndi kuima kwa mpirawu kamba koti timu ikamachita bwino simafunika kuima koma kumbali ina awonjezera mphamvu zina kuti atha kumachitabe bwino.
Timuyi ikadali pamwamba pa ligi pomwe ili ndi mapointsi 25 pa masewero asanu ndi anayi omwe yasewera mu ligiyi ya chaka chino.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores