KOMITI YAVOMEREZA MAYINA A PACHISANKHO CHA FAM
Komiti yaikulu yomwe ikuyang'ana za chisankho cha bungwe la Football Association of Malawi lavomereza mayina a anthu omwe anasankhidwa ndi mabungwe omwe amavota kuti akayimire pa chisankhochi.
Komitiyi imakumana loweruka kuti iunikire mayinawa ndipo yavomereza mayina awa:
PRESIDENT 1. Fleetwood Haiya 2. Walter Nyamilandu Manda
FIRST VICE PRESIDENT 1. Christopher Madalitso Kuyera 2. James Mwenda
SECOND VICE PRESIDENT 1. Dr Lameck Khonje 2. Othaniel Hara
EXECUTIVE MEMBERS 1. Daudi Ntanthiko 2. Chancy Gondwe 3. Patrick Kapanga 4. Bernard Harawa 5. Raphael Humba 6. Chimango Munthali 7. Muhammad Selemani
WOMENS REPRESENTATIVE 1. Felister Dossi 2. Mervis Mangulenje
Mu kalata yosainidwa ndi wapampando wa komitiyi, yapereka mphamvu kwa anthu omwe ali ndi vuto ndi mayinawa. Kuti akhonza kukaneneza kuti achotsedwe pa ndandandawu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores