"MASEWERO AKADALIPOBE NDIPO TIYESETSA" - MKANDAWIRE
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Red Lions, Malumbo Mkandawire, wati timu yake iyesetsa kulimbikira mmasewero khumi omwe atsala nawo kuti amalize ligi ya chaka chino ndi cholinga choti achoke kumunsi kwa ligiyi.
Mkandawire amayankhula izi atatha masewero omwe agonja 1-0 ndi Mighty Wakawaka Tigers pa bwalo la Kamuzu ndipo anati timu yake yaphonya mipata yochuluka. Iye wati ayesetsa mmasewero omwe atsala nawo kuti asatuluke mu ligi.
"Apapa zinthu zikuipadi komabe tidikire chifukwa masewero atsala angapo, ife tatsala ndi 10 nde tiyesetsa kuwauza anyamata kuti alimbikire ndi cholinga choti tichoke kumunsi komwe tiliko." Anatero Mkandawire.
Lions yatsakamira pa nambala 15 pomwe yakwanitsa kupeza mapointsi 18 pa masewero 20 omwe asewera mu ligi ya TNM.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores