Songwe ikugawa chipulumutso mu Supa ligi
Timu ya Songwe Border United ikadapitilizabe kugonja mu ligi ya TNM pomwe yagonja masewero achi 23 pa masewero 27 omwe asewera mu ligiyi pomwe agonja 2-0 ndi timu ya MAFCO pa bwalo la Champions lachitatu masana.
Timuyi inakwanitsa kuyimitsa MAFCO mchigawo choyamba koma inagoletsetsa mu mphindi makumi awiri zakumapeto kudzera mwa Zikani Sichinga ndi China Chirwa kuti igonje mmasewerowa.
Mphunzitsi wamkulu Edwin Kaonga anati timu yake inafooka mchigawo chachiwiri mpake inagonja koma inaonetsa kaseweredwe kapamwamba mchigawo choyamba.
''Tikadapitilirabe ndipo lamulungu tili ndi masewero ndi Silver Strikers nde tibwerera tikakonze mavuto athu kuti mwina tidzachite bwino pa masewerowa,'' anatero Kaonga.
Timuyi tsopano ili ndi mapoints okwana asanu ndi imodzi (6) pomwe yakwanitsa kupambana kamodzi, kufanana mphamvu katatu ndi kugonja ka 23 ndipo anatuluka kale mu ligiyi.
0882410060
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores