"TIMAYEMBEKEZERA ZAMBIRI PA ANYAMATAWA" - MWASE
Mphunzitsi watimu ya Mighty Mukuru Wanderers, Meke Mwase, wati timu yake yagonja kamba koti anyamata sanachite monga momwe amaonetsera pa zokonzekera komanso manjenje a goloboyi awapweteka.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 2-1 ndi timu ya FCB Nyasa Big Bullets kuti atuluke mu chikho cha FDH Bank ndipo wati sanasangale chifukwa samayembekezera zimenezi.
"Anyamata sanachite zimene timayembekezera chifukwa ku zokonzekera amachita bwino komanso goloboyi kukhala masewero ake aakulu anachita timanjenje." Anatero Mwase.
Iye wati timu yawo iyang'anabe chitsogolo kuti aone kuti ikhonza kuchita motani koma iye sizinamusangalatse poti samayembekezera zimenezi.
Timu ya Wanderers tsopano iyang'ane chidwi chawo ku mpikisano wa TNM Supa ligi pomwe akumane ndi Baka City lachinayi.
Zimachitika zagwa zatha look forward manoma
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores