"KUCHINYITSA ZITATU ZOKHA PA WANDERERS NDI CHILIMBIKITSO" - MKANDIRA
Mphunzitsi watimu ya Panthers, Innocent Mkandira, wati ndi chilimbikitso chachikulu kwambiri ku timu yawo kungogonjako zigoli zitatu zokha pa masewero omwe anakumana ndi Mighty Mukuru Wanderers poti osewera awo sangafanane ndi a Wanderers.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 3-0 kuti atuluke mu chikho cha Castel Challenge mu ndime ya matimu anayi ndipo wati iwo anayesetsa koma zavuta.
"Mutha kuona mchigawo choyamba tinayesetsa kuyimitsa Wanderers sitinachinyane koma mchigawo chachiwiri tinakanika kumaka bwinobwino nde atachinya choyamba anatibalalitsa kwambiri." Anatero Mkandira.
Iye wati komabe kutengera kukula Kwa timu ya Wanderers ndi luso la osewera atimuyi alili, kugonja ndi zigoli zitatu zokha ndi chilimbikitso chachikulu kwambiri.
Wanderers yafika mu ndime yotsiriza ndipo ikumana ndi wopambana pakati pa timu ya FCB Nyasa Big Bullets ndi Mzuzu City Hammers.
Nonse takutumizirani ndalama zomwe mwawina 👏👏
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores