"CHIPAMBANO CHITITHANDIZA KUFUFUTA ZONSE" - MTETEMERA
Mphunzitsi wogwirizira watimu ya Mighty Wanderers Macdonald Mtetemera wati timu yake ikuyenera kupeza chipambano pamwamba pa timu ya Blue Eagles chomwe chifufute kusachita bwino kwawo mu mipikisano ya CAF Champions League komanso mu Airtel Top 8.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo omaliza mu chigawo choyamba cha ligi ya FDH Premiership pa bwalo la Nankhaka mu mzinda wa Lilongwe loweruka masana.
Iye wati zolakwitsa zomwe anachita mu masewero omwe agonja ndi zomwe zinawapweteketsa ndipo ayesetsa kukonza zinthuzi cholinga choti achite bwino ndikumaliza mchigawochi pamtunda pa ligiyi.
"Zinthu zakedi sizinayende bwino kutengera kuti ndife timu yaikulu koma nkhani ndi kukambirana kuti zinthuzi tiziyiwale ndipo kupambana ndekuti kupereka chilimbikitsonso kuti tiyambirenso kuchita bwino," anatero Mtetemera.
Iye anati vuto la kusagoletsa zigoli ndi komwe kunachititsa kuti agonje mmasewero awo ndipo tsopano akonza zonse kuti ndi B
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores