MITHI, PETRO NDI MZUNDA ALIMBIRANA MPHOTO YA WOSEWERA WAPAMWAMBA
Osewera atatu omwe ndi Lameck Mithi wa Mighty Wanderers, Ernest Petro wa Silver Strikers komanso Webster Mzunda wa Blue Eagles alimbirana mphoto ya wosewera yemwe wasewera bwino kuposa aliyense mu mwezi wa May mu FDH Premiership.
Izi zadziwika pomwe bungwe la Super League of Malawi latulutsa ndandanda wa mayinawa lachinayi mammawa.
Mithi anakwanitsa kusewera masewero asanu ndi amodzi mu mweziwo omwe anayi anayamba ndipo awiri anachokera panja pomwe anamwetsa zigoli zisanu ndi kupambana mphoto yoti wasewera bwino imodzi.
Naye Petro anasewera masewero asanu ndi amodzi ku Silver Strikers pomwe anapambana mphoto ya osewera wapamwamba pa masewero kawiri.
Mzunda nayenso anapambana mphoto ya osewera wapamwamba mu masewero kawirinso pa masewero asanu ndi amodzi omwe wasewerera Blue Eagles.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores