CHITIPA YAGONJA KOYAMBA PAKHOMO
Timu ya Chitipa United yagonja koyamba pakhomo mu ligi ya FDH Premiership chaka chino pomwe yagonja 4-0 ndi timu ya Mighty Wanderers pa bwalo la Chitipa lamulungu.
Timuyi inali isanagonjeko pakhomo chiyambireni ligi koma kugonja onse akoyenda ndipo inagoletsetsa zigoli ziwiri mu mphindi khumi kupangitsa Wanderers kusewera mtima uli mmalo.
Mphunzitsi watimuyi, Kondwa Ikwanga, wati zigoli zachangu kwambiri zomwe anagoletsetsa ndi zomwe zawapangitsa kuti avutike kwambiri mu masewerowa.
"Mukati muone zigoli ziwiri zoyamba zija, palibe chimene tinapanga basi kungowapatsa zomwe zili zoipa kwambiri nde poti zimachitika mu mpira, tibwerera kuti tikakonze zolakwika zathu," anatero Ikwanga.
Iye walimbikitsanso otsatira timuyi kuti asadere nkhawa kamba koti timuyi iyambiranso kuchita bwino posachedwapa.
Chitipa yakwanitsa kupambana masewero awiri ndi kugonja anayi ndipo ali ndi mapoints okwana asanu ndi imodzi pa nambala 13 mu ligiyi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores