CHITIPA IKUCHITA BWINO PAKHOMO
Timu ya Chitipa United yakwanitsa kupambana masewero awo onse omwe ikusewera pakhomo pomwe yagonjetsa timu ya Civil Service United 1-0 kuti ifike pa nambala 7 mu FDH Premiership loweruka.
Timuyi yagonja kawiri koyenda koma ikukwanitsa kupambana masewero apakhomo zomwe zawathandizira kuti akhale ndi mapoints asanu ndi imodzi mu ligi.
Mu masewerowa, Zenga Manda anagoletsa chigoli chake chachiwiri mu ligi kuti akwanitse kupeza chipambano ndi kukhala oyamba kugonjetsa Civil.
Mphunzitsi wamkulu, Kondwa Ikwanga, wati ndi wokondwa kwambiri koma amafunitsitsa kuti apeze zigoli zodutsira ziwiri mmasewerowa.
"Ineyo Chimwemwe changa ndi chosawerengekatu chifukwa anyamata asewera bwino kwambiri ngati momwe tinakonzekerera ndithu," iye anatero.
Iye koma anati ayesetsa kuti azikwanitsanso kupeza zipambano koyenda osati pakhomo pokha komabe ndi zabwino kuti pakhomo akupagwiritsa bwino ntchito.
Chitipa ili pa nambala 7 mu ligi pomwe ili ndi mapoints asanu ndi imod
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores