CHITIPA YAPEZA CHIPAMBANO CHOYAMBA MU LIGI
Timu ya Chitipa United yapeza chipambano chawo choyamba mu ligi ya chaka chino itagonjetsa Blue Eagles 1-0 pa bwalo la Chitipa loweruka masana.
Joseph Mbaga anamwetsa chigoli chokhacho cha mmasewerowa mu chigawo chachiwiri kuti timuyi ipeze chipambano kamba koti mmasewero awo oyamba anayamba ndi kugonja.
Mphunzitsi watimuyi Kondwa Ikwanga wati timu yake inapita mu masewerowa kuti ikwanitse kupeza chipambano basi kuti ayambe ulendo wawo wamu ligi.
"Lero timangomenya basi kuti tipeze chipambane, anzathu aja amenya mpira ndipo amatipanikiza koma timangofuna basi tipambane kuti tilimbe mtima pomwe tikupita chitsogolo poti kuyamba ndi kovuta ndiye zatheka," anatero Ikwanga.
Iye anati pali zambiri zomwe zikufunika kukonzedwa mu timuyi kuti izikwanitsa kuchita bwino pomwe wati sanasewere bwino kusiyana ndi masewero awo oyamba ndi Masters.
Timuyi tsopano yafika pa nambala yachisanu mu ligi pomwe ili ndi mapoints atatu pa masewero awiri mu ligi y
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores