JOSEPHY APEZEKA PA MASEWERO NDI HAMMERS
Timu ya Silver Strikers ikhala ndi katswiri wawo omwetsa zigoli, Andrew Josephy, pa masewero omwe asewere ndi timu ya Mzuzu City Hammers mu chikho cha Castel.
Mphunzitsi watimuyi, Peter Mgangira, ndi yemwe watsimikiza za nkhaniyi pomwe amafotokoza momwe akonzekerera maewerowa.
Iye wati akuyembekera kukumana ndi masewero ovuta pomwe masewero amu chikho amakhala ovuta kwambiri.
"Tikukumana ndi timu yabwino yoti ndikudabwanso kuti inatuluka bwanji mu ligi komano anyamata onse alipo ndipo akudziwa kufunikira kopambana masewerowa," iye anatero.
Matimuwa akukumana mu masewero otsiriza amu ndime ya matimu 16 amu mpikisanowu ndipo wopambana akumana ndi Mighty Wanderers mu ndime yamatimu asanu ndi atatu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores