"SITITENGERA MAYINA KOMA KASEWEREDWE" - FAZILI
Mphunzitsi watimu ya Scorchers, Lovemore Fazili, wadandaula kuti osewera ena omwe amatumikira matimu akunja kwa dziko lino komanso ena okhalitsa kutimuyi sakuseweranso mofikira mulingo wofunikira kuti timuyi ichite bwino.
Iye amayankhula izi mdziko la Kenya kutsatira kutha kwa mpikisano wa FIFA World Series omwe Malawi inathera pamapeto penipeni.
Iye wati pomwe akupita ku mpikisano wa Womens African Cup of Nations, osewera ena omwe asewera kwambiri timuyi sadzatengedwa kamba koti sakuseweranso bwino.
"Tikamatenga osewera opita ku WAFCON sititengera mayina koma momwe akusewerera chifukwa ena akufooka. Mwina sanali bwino chabe koma aliyense akuyenera kuonetsa pa bwalo," anatero Fazili.
Iye watinso osewera ena akutha zaka zitatu kapena zinayi ndi timuyi ndipo amayenera kuti akhazikika koma akukanikabe kuti atero.
Izi zadzanso pomwe anthu ochuluka adandaula ndi kaseweredwe ka osewera ena omwe amaoneka kuti odalilika mu timuyi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores