"TIKUFUNIKA KUGOLETSA ZIGOLI ZAMBIRI" - FAZILI
Mphunzitsi watimu ya Scorchers, Lovemore Fazili, wati akonzekera zopita kutsogolo kwambiri pomwe akukumana ndi Lesotho cholinga choti adzagoletse zigoli zochuluka.
Iye amayankhula patsogolo pa masewerowa omwe aliko loweruka ndipo wati zigoli zochuluka ndi zothandizanso kuti adzafike mu ndime ya matimu anayi mpikisanowu.
Iye wati kubwera kwa Vanessa Chikupira kuwathandizire kuti akwanitse kupata zigolizi ndi ukadaulo wa katswiriyu.
"Tikukonza zomwe tinalakwitsa ndi South Africa komanso kulimbikira zabwinozo nde tidzayesetsa kuti tidzagoletse zigoli zochuluka kuti mwina zidzatithandize patsogolo," anatero Fazili.
Malawi inayamba ndi kugonja masewero awo 2-0 ndi South Africa ndipo Lesotho nayo inagonja 3-1 ndi Angola.
Matimu onse awiri alibe point iliyonse mu gulu A ndipo timu yomwe ithere pamtunda idzafika mu ndime ya matimu anayi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores