Timu ya Karonga United yalengeza kuti Audlow Makonyola ndiye mphunzitsi wawo mu zaka ziwiri zikudzazi kutsatira kusaina mgwirizano ndi timuyi.
Timuyi yalengeza za nkhaniyi lachitatu pomwe amasakasaka mlowammalo wa Oscar Kaunda yemwe wachoka kutimuyi.
Poyankhula atasaina mgwirizano wake, Makonyola wati akuyembekeza kukhala ndi nthawi yabwino kwambiri kutimuyi poti ndi yabwino.
"Ndili ndi chiyembekezo kuti tizikhala tikusewera mwapanwamba. Khumbo langa ndi loti tithere mu matimu atatu oyambilira mu ligi," iye anatero.
Makonyola anali ku timu ya Mitundu Baptist yomwe wayichotsa mu Division 1 ya chigawo chapakati mpaka kuyilowetsa mu ligi yaikulu ya mdziko muno.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores