"Tinakonzekera kusewera kulikonseko" - Msakakuona
Mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, De Klerk Msakakuona, wati timu yake sinakhudzidweko ndi kusinthasintha kwa mabwalo osewerera masewero awo amu ndime ya matimu anayi a chikho cha Castel poti amadziwabe kuti adzasewera kumathero a sabata ino.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero a timuyi ndi Goshen City Dedza Dynamos pa bwalo la Kamuzu ndipo wati iwo ali okonzeka kusewera masewerowa.
"Tinakonzekera bwino kwambiri ndipo palibe yemwe ali ovulala, kwangotsala kusankha odzayamba masewerowa koma takonzekera bwino kuti tichite bwino tifike ndime yotsiriza," iye anatero.
Iye wati timu iliyonse tsopano ili ndi kuthekera kofika mu ndime yotsiriza ndipo Dynamos ndi timu yabwino koma akukhumbira atachita bwino poti ndi timu yaikulu.
Ngati angapambane, Eagles idzakumana ndi wopambana pakati pa FCB Nyasa Big Bullets ndi Mzuzu City Hammers mu ndime yotsiriza.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores