Nyirenda waonjezera mgwirizano wake ku Wanderers
Katswiri wotseka kumbuyo kutimu ya Mighty Wanderers, Emmanuel Nyirenda, waonjezera mgwirizano wake kutimuyi pomwe afike mu 2027 akutumikirabe timuyi.
Timuyi yalengeza za izi lachiwiri ku mmawa kuti mgwirizano watsopanowu womwe ndi wa zaka ziwiri udzatha mu December 2027.
Nyirenda anabwera ku Manoma mu 2023 kuchokera ku Mighty Tigers ndipo mu chaka cha 2025 ndi chomwe anaonetsa luso pokhala wodalilika kumbuyo kwa timuyi.
Iye wathandizira kwambiri timuyi kutenga ukatswiri wa ligi koyamba mu zaka 8.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores