Kamanga waonjezera mgwirizano wake ku Wanderers
Katswiri wosewera pakati kutimu ya Mighty Wanderers, Mphatso Kamanga, waonjezera mgwirizano wake ndi zaka zitatu kutimuyi lolemba.
Timuyi yatsimikiza za nkhaniyi kudzera pa tsamba lawo la mchezo pomwe iye akakhalebe kufika mpaka mu mwezi wa December mu 2028.
Osewerayu sanapezeke danga lenileni losewera mu timuyi chichokereni ku Karonga United mu 2023 ndipo chaka chino anali wovulala kwa ligi yonse koma atha kuoneka mu chikho cha Castel.
Iye wapambanako chikho cha Castel Challenge komanso Supa ligi ndi Manoma mu kukhala kwake.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores