Wanderers ikufuna ku Bingu
Timu ya Mighty Wanderers yalembera bungwe la Super League of Malawi kupempha kuti masewero awo ndi Kamuzu Barracks akaseweredwe pa bwalo la Bingu osati pa Balaka.
Timuyi yapanga chiganizochi ati pofuna kuti masapota ambiri omwe akonzekera kuti adzaone timuyi ikupatsidwa chikho asakathinane potengeranso kuti bwalo la Balaka ndi laling'ono.
Masewerowa anayikidwa ku Balaka kamba koti ma bwalo onse mu mzinda wa Blantyre kudzakhala masewero ndipo bwalo lapakhomo lachiwiri la Wanderers ndi Balaka.
Padakali pano bungweli silinayankhepo pa pempholi koma atsimikiza kuti kalatayo yawafika.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores