Wanderers itha kutenga ligi loweruka
Timu ya Mighty Wanderers ikhonza kukhala akatswiri a TNM Supa ligi loweruka ngati angakwanitse kugonjetsa Moyale Barracks ndikupemphereranso kuti FCB Nyasa Big Bullets itaye mapoints pa masewero awo.
Manoma akulowa mu masewero awo ndi Moyale akudziwa kuti chipambano chokha ndi chomwe akufunikira kuti mwayi wawo wotenga ligi ukule ndipo ngati Bullets ingagonje kapena kufanana mphamvu ndi Tigers akhonza kutenga ligi.
Wanderers inalepherana 1-1 ndi Moyale Barracks mchigawo choyamba ndipo mu ligi ya chaka chatha anagonja 2-1 pa bwalo la Kamuzu ndi Moyale yomweyi.
Iyo ili ndi mapointsi okwana 65 pa zipambano 19, kufananitsa mphamvu kasanu ndi katatu ndi kugonja kamodzi mu ligiyi, mapointsi atatu pamwamba pa Bullets.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores