BULLETS YAONJEZERA NZERU ZA APHUNZITSI AWO
Timu ya FCB Nyasa Big Bullets inachititsa maphunziro a aphunzitsi atimuyi kuyambira timu yaikulu, yaing'ono, yachisodzera komanso ya amayi pofuna uonjezera upangiri wa aphunzitsiwa.
Maphunzirowa anachitika kutsatira mgwirizano wa timuyi ndi sukulu yosula aphunzitsi a mpira ya SK Academy ys mdziko la Britain ndipo amaphunzitsa ndi a Dan Quigley ndi a David Ramjee lachiwiri ku Blantyre.
Maphunzirowa anapereka upangiri kaphunzitsidwe, kuika nzeru zapadera pa masewero, kaganizidwe komanso mphamvu ndipo sukuluyi yati aphunzitsi anali ndi njala yofuna kuphunzira kwambiri ndipo zithandize kuti akhale ndi osewera abwino omwe aziwathandiza kutenga zikho.
Mphunzitsi watimu yaikulu, Peter Mponda, wati maphunzirowa anali opambana omwe awathandizire pomwe akuyenda mu masewero akumapeto amu ligi ya TNM.
''Linali tsiku lopambana kwa aphunzitsi a Bullets ndipo maphunzirowa atitsuka upangiri wathu pa kuganiza, mphamvu, kaphunzitsidwe ndi kuwerenga masewer
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores