''TIVOMEREZEDI KUTI ATIPWETEKA A CRECK'' - CHIRWA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Gilbert Chirwa, wati timu yawo inali ndi mavuto ochuluka kwambiri pa masewero awo ndipo avomereza kuti apwetekedwa pa masewerowa.
Iye amayankhula kutsatira kugonja 2-0 pa masewero omwe anali pa bwalo la Aubrey Dimba ndipo wati izi zaika timuyi pa phuma kwambiri pa ntchito yokatenga ligi.
''Lero sitinasewere ngati timu ndipo tivomereze kuti atipweteka. Zimadabwitsadi kuona osewera momwe analili chifukwa timasowekera zambiri komabe tikonza tikhala nawo pansi ndipo zonse ziyenda bwino,'' anatero Chirwa.
Iye wavomerezanso kuti anyamata abwino-abwino mu timuyi akuchepa koma ndi vuto loti sangalikonze padakali pano.
Bullets ikadali pa nambala yoyamba ndi mapoints 56 pa zipambano 18, kufanana mphamvu kawiri ndi kugonja kasanu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores