''TIKUMENYA NDI TIMU YABWINO KOMA SITIKUYIOPA'' - MGANGIRA
Mphunzitsi watimu ya Silver Strikers, Peter Mgangira, wati timu yake yakonzeka kukumana ndi timu ya Mighty Wanderers ndipo sapita mophweka motengera kuti anawagonjetsa mu chikho cha FDH Bank posachedwapa.
Iye amayankhula patsogolo pa masewerowa omwe ali pa bwalo la Bingu loweruka masana ndipo wati timu iliyonse yomwe amakumana nayo amayipatsa ulemu koma osati kuyiopa.
''Tikukumana ndi timu yoti ili ndi aphunzitsi abwino komanso osewera abwino ndipo siyinagonjepo mu ligimu koma chipambano ndi chabwino kwa ife chifukwa chitipatsa mphamvu komanso kuchepetsa mpata kwa iwowo,'' anatero Mgangira.
Iye wati kupuma komwe kunalipo kuchoka sabata yatha kwakhala bwino poti anyamata apuma tsopano malingana kuti masewero amaseweredwa pafupipafupi.
Timuyi ili pa nambala yachitatu ndi ma points 40 pa masewero 20 omwe yasewera mu ligi ndipo mu chigawo choyamba anathera 1-1.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores