Osewera akale, aphunzitsi akukayikira kuti Yann Kouakou si m'Malawi
Osewera akale ena a mdziko kuno komanso aphunzitsi a mpira wamiyendo ayamba kufufuza za kabweredwe ka Yann Kouakou yemwe ali ndi timu ya Flames kutsatira malipoti oti makolo ake onse si aku Malawi.
Anthuwa analumana mutu atamvetsedwa kuti osewerayu yemwe mphunzitsi Kalisto Pasuwa wayenda naye mdziko la South Africa si wa mdziko muno poti mayi ake ndi aku Zimbabwe pomwe abambo ake ndi aku Ivory Coast.
Iwo akukayikira njira zomwe osewera ngati awa ayambira kutulukira ndipo akukhulupilira kuti akutenga malo omwe a malawi eni ake akanakhalapo.
Malingana ndi zomwe tapeza, akuluakuluwa akumana lolemba pomwe apatsidwe umboni womaliza womwe ataupereke ku dziko lonse kuti lidziwe.
Kouakou amasewera mdziko la Gilbratar mu timu ya Europa Point ndipo malingana ndi FAM, iye ndi wa mdziko muno.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores