Masewero pakati pa Silver Strikers Ladies ndi MDF Lioness omwe amayenera kuseweredwa pa bwalo la Silver alephereka.
Masewerowa akanika kuseweredwa kamba koti pabwaloli panadzadza madzi kamba ka mvula yomwe inagwa mu mzinda wa Lilongwe.
Ndipo akuluakulu oyendetsa ligi ya National Bank of Malawi National Womens Premiership awona kuti ndi kwabwino kuti masewerowa asachitike ndipo mmalo mwake adzakhalapo lolemba nthawi ya 10 koloko.
Chokoma china ndi chakuti matimu awiri onse amachokera ku Lilongwe komweku.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores