Khungwa watsogola pa masewero osachinyitsa
Wotchinga pagolo watimu ya Mighty Wanderers, Dalitso Khungwa, tsopano watsogola pa masewero omwe magoloboyi akhala osachinyitsa pomwe wasewera masewero 11 osagoletsetsako chigoli.
Khungwa wapitilira anzake ena anayi lachitatu masana atakhala osachinyitsa pomwe Mighty Wanderers yagonjetsa Songwe Border United 2-0 mu ligi ya TNM.
Iyeyu tsopano wasewera masewero okwana 13 ndipo wachinyidwako zigoli ziwiri zokha ndi Alfred Chizinga wa Karonga United pa penate komanso Pius Saka wa Blue Eagles.
Goloboyi wa Chitipa United, Jacob Anyandwile sanagoletsetse mu masewero 10 pa 16 omwe wasewera ndipo Innocent Nyasulu wa FCB Nyasa Big Bullets sanagoletsetsenso mmasewero 10 a masewero ale 17, Rahaman John wa Civil sanachinyitse pa maseweronso 10 pa 18 ndipo McLean Mwale wa Karonga United sanachinyitsenso mmasewero khumi pa 21 omwe wagwirira.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores