Osewera odutsa 100 asintha matimu
Bungwe loyendetsa ligi yaikulu ya m'dziko muno la Super League of Malawi lati osewera odutsa 100 asintha matimu pa msika wogula ndi kugulitsa osewera wa pakati pa ligi pomwe tsopano watsekedwa.
Mlembi wamkulu wa bungweli, Williams Banda, wati msikawu unali wopambana pomwe osewera ena agulidwiratu, ena apita pa ngongole pomwe ena mwaulere poti mgwirizano wawo unatha.
Iye wati matimu akuyenera kupanga zimene anagwirizana pogulitsana osewera ndipo kupanda kutero udzakhala mlandu.
"Tichenjezenso kuti osewera omwe sanapatsidwe zikalata zoti atha kukasewera timu ina sasewera mu Chigawo chachiwiri cha ligiyi," Anatero Banda.
Bungweli lapempha osewera ndi matimu kusewera ligiyi mopanda zitopotopo ndi zosokoneza cholinga iyende bwino mpaka pamapeto.
Msikawu unatsegulidwa pa 08 August 2025 ndipo tsopano watha pa 04 September 2025.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores