"Ndine wokondwa poti anyamata asewera bwino" - Kananji
Mphunzitsi watimu ya Creck Sporting Club, Eliya Kananji, wati wasangalala ndi mmene timu yake yasewerera ndi timu ya Mighty Wanderers ndipo ndi wokhutira kamba kopeza point imodzi pa masewerowa.
Iye amayankhula atatha masewero omwe alepherana 0-0 pa bwalo la Balaka lachitatu ndipo wati timu yake inakonzekera bwino mmasewerowa ndipo anyamata achita mofanana ndi momwe anawauzira.
"Tinawauza kuti aliyense agwire osewera wake chifukwa kuwalora a Wanderers kuti akhale ndi mpira akhonza kukupweteka nde ndine wasangalala ndi momwe asewera ndipo point imodzi sizinaipe kwambiri." Anatero Kananji.
Iwe wati ayesetsa kuti azitolera mapointsi atatu mu masewero awo kamba koti matimu enanso omwe ali pansi pano abwera moopsa kumtundako.
Timuyi tsopano ili pa nambala 9 ndi ma points okwana 20 pomwe yapambana kasanu, kufanana mphamvu kasanu ndi kugonja kasanu ndi kawiri.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores