"Titha kukhala oyamba kugonjetsa Wanderers" - Kananji
Mphunzitsi watimu ya Creck Sporting Club, Eliya Kananji, wati timu yake yakonzekera bwino kwambiri masewero awo ndi Mighty Wanderers ndipo nzotheka kukhala oyamba kuyibandula Wanderers mu ligi ya chaka chino.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo omwe ali pa bwalo la Balaka lachitatu masana ndipo wati ndi mmene akonzekerera akutha kuona atagonjetsa Manomawa lero.
"Ndi masewero ovuta poti tikukumana ndi Wanderers yomwe ndi timu yaikulu Koma sitikuyiopa poti tikusewera mulingo umodzi nde sitikuchita mantha chifukwa mmene takonzekerera titha kukhala oyamba kuyigonjetsa Wanderers." Anatero Kananji.
Iye wati wawauza anyamata ake kuti akakapeza mwayi wa chigoli asakanyengerere ndipo azikamenyera pagolo chifukwa Ilo nde vuto lomwe timuyi akhala akuchita.
Creck ikulowa mmasewerowa ili ndi ma points 19 omwe anawapeza pa zipambano zisanu, kufanana mphamvu kanayi ndi kugonja kasanu ndi kawiri pa nambala 10 mu ligiyi.
📸: Creck media
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores