NKHANI
Msungichuma wa Komiti ya masapota a timu ya Mighty Wanderers ku Chigawo cha kummwera, Clement Chimangeni wapereka ndalama yokwana K300,000 kwa atsikana a timuyi poyamikira momwe akuchitira.
Iye anachita izi kutsatira kugonjetsa timu ya Kukoma Ntopwa Queens 0-1 sabata yatha mu ligi ya National Bank of Malawi National Women's Premiership
Timuyi yakwanitsa kupambana masewero atatu onse akoyenda pa masewero anayi omwe yasewera kuti ikhale pa nambala yachinayi mu ligiyi ndi mapointsi okwana asanu ndi anayi (4).
Ieo anagonjetsa Moyale Sisters 2-0, Topik Academy 3-1 komanso Ntopwa 1-0 ndi kugonjako 2-0 pakhomo ndi Ascent Academy ndipo akutsalira ndi ma points atatu pa timu ya Silver Women komanso kufanana mapointsi ndi Ntopwa komanso Ascent.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores