Mpinganjira: Tiyesetsa kuti tizipambana masewero
Mphunzitsi watimu ya Mighty Wanderers, Bob Mpinganjira, wati ndi wosangalala kwambiri kuti akuluakulu atimuyi amukhulupilira kuti atha kutsogolera timuyi ndipo ayesetsa kuti izipeza zotsatira zabwino.
Iye amayankhula atatha kusaina mgwirizano wa chaka chimodzi kutsimikiza kuti tsopano ndi mphunzitsi watimuyi ndipo anati ayesetsa kugwira ntchito.
"Nkhani ndi kuwina masewero omwe tizisewera nde ndi aphunzitsi anzanga tiyesetsa kuti tizichita bwino." Anatero Mpinganjira.
Mphunzitsiyu anali wogwirizira kutsatira kuchoka kwa Meke Mwase ndipo anakwanitsa kupambana chikho cha Castel mu 2024.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores