Henderson walonjeza zabwino ku Bullets
Katswiri wotseka kumbuyo watsopano ku timu ya FCB Nyasa Big Bullets, Chikumbutso Henderson, wati akuyembekeza kusewera bwino kuposa momwe amachitira kutimu yomwe wachoka ndipo anthu ayembekezere zabwino.
Iye amayankhula atatha kusaina mgwirizano wa zaka ziwiri kuchokera ku timu ya Mzuzu City Hammers ndipo wati ndi okondwa kamba koti wapita ku timu yaikulu.
Iye wati akukhulupilira kuti apeza upangiri watsopano ku timuyi womwe upititse patsogolo kwambiri luso lake kumpira.
"Tikumana ndi anthu atsopano omwe andiphunzitse zambiri zomwe zindithandize kupita patsogolo ndi zina zomwe ndikudziwa kale nde masapota andilandire kuti tigwire ntchito." Iye anatero.
Henderson wakhala katswiri mbambande kutimu ya Mzuzu City Hammers pomwr mu chaka cha 2024 anayithandiza kuthera mu matimu anayi amu TNM Supa ligi komanso kufika mu ndime yotsiriza ya Castel Challenge Cup.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores