SULOM YALONJEZA KUKONZA ZAMBIRI
Bungwe la Super League of Malawi lalonjeza kuti mu ligi ya chaka cha 2025 akonza mmene ndandanda wa masewero umapangidwa komanso kaloweredwe ka mmabwalo kamakono pofuna kuti masewero aziyenda bwino.
Mtsogoleri wa bungweli, Colonel Gilbert Mitawa, amayankhula pomwe amaunikira momwe ligi ya 2024 yayendera ndipo wati inayenda bwino ndipo mpikisano unali wabwino.
Koma iwe wati mavuto a ndandanda wa osewera awupange ukhale wamakono pa kompyuta cholinga choti iziyenda bwino komanso kugula tikiti pa lamya ya mmanja.
"Izi zithandiza kuti ndalama zisamabedwe ndipo matimu komanso osewera omwe amagwira ntchito okha azipeza phindu." Anatero Mitawa.
Iye wapemphanso anthu kuwafikira a bungweli ngati zinthu zina zikulakwika cholinga choti aziyenda mu njira yokomera anthu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores