NKHANI
Timu ya Silver Strikers yakweza udindo katswiri wawo wakale, Peter Mgangira, kuti akhale mphunzitsi wamkulu kulowa mmalo mwa Peter Mponda yemwe wachoka kutimuyi.
Malingana ndi tsamba la Wa Ganyu latsimikiza za chiganizochi lachisanu masana kuti timuyi sipita patali kukasaka mphunzitsi wina.
Mgangira wakhala nthawi yaitali kutimuyi pomwe wakhalako wachiwiri kwa Dan Kabwe, Peter De Jongh komanso Peter Mponda mu zaka zapakati pa 2021 mpaka 2024.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores