"TIMAFUNA ENA AMVEKO KUTI KUTENGA CHIKHO KUMAKOMA BWANJI" - CHIGOGA
M'dindo wamkulu kutimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Albert Chigoga, wati matimu ayembekezere fumbi mu chaka cha 2025 pomwe chaka chino amangofuna matimu ena alaweko msuzi wa zikho ndipo chaka cha mawa zikubwerera ku mapale.
Iye amayankhula pa mwambo womwe timuyi inali kupereka mphoto kwa osewera omwe achita bwino mu chaka cha 2024 lolemba usiku.
Iye wati mwambowu umayenera kuchitika kutimuyi chaka chilichonse kutimuyi posatengera ndi mmene achitira mu chaka kuti athokoze ntchito ya osewera ndi aphunzitsi.
Iye wati timuyi ili mkati mokonza kuti chaka cha mawa adzapitilire kuchitanso bwino mu zikho zonse.
"Ine ngati CEO ndikuwauza anthu kuti kukhale kukuchitika zambiri kufikira nthawi yomwe zokonzekera ziyambe kuti tibwerere mchimake ndipo mu 2025 kuli fumbi apa timangofuna kuti ena alaweko mmene zimakomera kutenga chikho." Anatero Chigoga.
Pa mwambowu, Richard Chimbamba anasankhidwa kuti ndi wotchinga pagolo
wapamwamba, Nickson Nyasulu wakumbuyo, Lloyd Aaron anali wapakati, Babatunde Adepoju nde wakutsogolo, Chikumbutso Salima ndi yemwe wazitolera kwambiri ndipo Nyasulu wasewera kuposa onse mu chakachi
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores