KAFOTEKA WAMEMA ANTHU KU PHWANDO LOTSALA MU LIGI
Mphunzitsi watimu ya FOMO FC, Elvis Kafoteka, wapempha anthu ozungulira ku Mulanje kuti afike mwa unyinji pa bwalo la Mulanje Park masana a loweruka kuti akasapotere timuyi mu masewero omwe awathandizire kuti atsalebe mu ligi.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi timu ya Karonga United masana a loweruka ndipo wati masewerowa ndi ovuta kwambiri chifukwa timu yomwe akusewera nayo ndi yodziwanso.
Iye wati kugonjetsa Silver Strikers sikukutanthauza kuti angagonjetse Karonga ndipo akuyenera kudzalimbikira kwambiri mchifukwa chake wapempha anthu kudzachemerera timuyi.
"Tikupempha Mulanje yonse kuti adzabwere timuyi ndi yawo adzayimbe adzasokosere adzakhala osewera wachi 12 nde Karonga idzaone nyanja ya yellow lowerukali." Anatero Kafoteka.
Timuyi itsala mu ligi pokhapokha ngati ingapambane masewero awo koma kupanda kutero, masamu adzagwira ntchito poti nayo Bangwe All Stars ndi Chitipa United ali maso pomwepo.
FOMO 2 : 1 Karonga
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores