"KHUMBO LATHU TIKAFIKE NDIME YOTSIRIZA" - KAFOTEKA
Mphunzitsi watimu ya FOMO, Elvis Kafoteka, wati timu yake ili ndi loto lofika mu ndime yotsiriza ya mpikisano wa Castel Challenge Cup ndipo akufunikira kuonjezera mphamvu zawo kuti akwanilitse lotoli.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi timu ya Bangwe All Stars pa bwalo la Mpira ku Blantyre ndipo wati akudziwa kuti akhale masewero ovuta poti akukumana ndi timu yomwe ikuchita bwino komanso kuti ili patsogolo pawo mu ligi.
Iye anati, "Ndi loto la mphunzitsi wina aliyense kufika mu ndime yotsiriza ya mpikisanowu nde tikaphatikiza loto limeneli komanso osewera kulota zomwezi zithandiza kuti tichite bwino." Anatero Kafoteka.
Pa mikumano iwiri ya matimuwa mu ligi, FOMO inapambana masewero onse mu ligi koma matimuwa ali pa nkhondo yoti asatuluke mu ligi pomwe mapointsi awiri akusiyanitsa matimuwa.
Opambana pakati pa matimuwa akuyenera kukumana ndi Mighty Mukuru Wanderers mu ndime ya matimu asanu ndi atatu a mpikisanowu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores