"NAYENSO NKHAKANANGA WATENGAPO GAWO" - KAMANGA
Mphunzitsi watimu ya Kamuzu Barracks, Charles Kamanga, wadandaula kuti anthu amaloza chala timu ikagonja koma mmene anyamata ake aphonyera sizikufunika mphunzitsi komanso kuti Geoffrey Nkhakananga anapereka penate yabodza.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 1-2 ndi timu ya MAFCO pa bwalo la Nankhaka masana a loweruka ndipo wati wavomereza kwakukulu kuti timu yake sinasewere bwino ndipo agonja.
"Kugonja kopweteka kwambiri ndipo inuyo atolankhani ndinu mumafalitsa mutha kuona mmene anyamata amaphonyera tiziti zikufunanso mphunzitsi? Masewero alero tangowapatsa a MAFCO, asewera bwino komabe ifeyo zativuta tivomere." Anatero Kamanga.
Iye wati aonetsetsa kuti masewero awo achite bwino omwe atsala nawo kuti mwina angathe kuthera pabwino mu ligiyi.
Kamuzu Barracks ili pa nambala yachisanu ndi chitatu (8) pomwe ili ndi mapointsi okwana 37 pa masewero pa masewero 28 omwe yasewera mu ligi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores