"KULUZA UKU KWATIBWENZERETSA MMBUYO" - MWASE
Mphunzitsi watimu ya Mighty Mukuru Wanderers, Meke Mwase, wadandaula ndi kugonja kwa timuyi ndi timu ya FCB Nyasa Big Bullets pomwe wati mwayi wawo wolimbirana ligi watsikiratu.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 1-2 pa bwalo la Kamuzu loweruka masana ndipo wati anyamata ake anakanika kuchita zomwe anauzidwa mchigawo choyamba mpake anapezetsa zigoli.
"Tagonja zativutadi anali masewero ovuta kwambiri omwe tinayamba bwino koma anyamata athu amangolakwitsana okhaokha kupangitsa kuti tipezetse zigolizo, si momwe tinagwirizanirana kuti tisewere mchigawo choyamba." Anatero Mwase.
Iye wati abwerera kukakonza mavuto omwe awaona mmasewerowa koma tsopano mwayi wolimbirana ukatswiri wa ligi ndi wotsika kwambiri.
Timuyi ikadali pa nambala yachiwiri mu ligi pomwe ili ndi mapointsi okwana 44 pa masewero 23 omwe yasewera chaka chino.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores