"SITINATULUKIRETU MWINA NDI OYIMBIRA ABWINO TIDZAPAMBANA" - BUNYA
Mphunzitsi watimu ya Premier Bet Dedza Dynamos, Andrew Bunya, wati timu yake ilinso ndi mphindi zina 90 zomwe timuyi ikhonza kumenyera nkhondo kuti ipitilire mu mpikisano wa Airtel Top 8 pomwe ngati atakumana ndi oyimbira abwino atha kudzatulutsa Silver Strikers.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 4-1 ndi timu ya Silver Strikers pa bwalo la Silver lachitatu ndipo wati timu yake sinatulukebe mu mpikisano.
"Tili ndi mphindi zina 90 ku Dedza zoti titati takonza mavuto athu tikhonza mwina kukachita bwino, sitinatuluke mwina titha kukakumana ndi oyimbira abwino omwe akakwanitse kuyimbira masewero athu kenako ndi kufika mu ndime ina bwinobwino." Anatero Bunya.
Iye anadandaula ndi chigoli chachiwiri chomwe Silver inapeza ATI poti mpirawo unaponyedwa mmalo olakwika ndipo masewerowa anayimako kwa mphindi zingapo pofuna kuti chigolichi chikanidwe.
Opambana pakati pa matimu awiriwa adzakumananso ndi opambana pakati pa
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores