"TINAGWIRIZANA KUTI ASADUTSE NAMBALA 11 MCHIGAWO CHOYAMBA" - MALOYA
Mlembi wamkulu wa timu ya FOMO FC, Jimmy Maloya, wati timu yake yatheka mgwirizano wa aphunzitsi awo, Gilbert Chirwa ndi Luckson Mauluka Nyoni kamba kosakwanilitsa zomwe anauzidwa.
Iye amayankhula atatha kutsimikiza za kuthetsedwa mgwirizano wa aphunzitsiwa omwe anayimitsidwa masabata apitawo ndipo Iwo anati akadakambirana.
"Pa zokambirana zawo ndi akuluakulu atimuyi akanika kumvana zomwe zachititsa kuti athetse mgwirizanowu koma chomwe chinalipo ndi choti anasayinirana kuti chikamatha chigawo choyamba adzakhale osafika mpaka nambala 11 mu ligi." Anatero Maloya.
Iye wati padakali panopa, Elvis Kafoteka apitiliza kutsogolera timuyi ndipo ngati atenge pepala lake la CAF B mu November muno, atha kudzakhala mphunzitsi wamkulu koma mbali ina azisakabe poti Pano siwoyenera.
FOMO inathera pa nambala 13 mchigawo choyamba ndipo padakali panopa ili pomwepo ndi mapointsi okwana 18 pa masewero 19.
Wolemba: Hastings Wadza Kas
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores